Pages

Thursday 31 May 2012

Chaminade yatisulila anthu aphindu-Mtumbuka


Wolemba: Pius Nyondo
8:00 m’mawa, 26 Meyi, 2012. Anthu mazana mazana ochokera kumadera osiyanasiyana m’dziko muno adali kukhamukira ku Chaminade sekondale sukulu ku Karonga. Ambiri mwa anthuwa amaoneka okalamba, ena amayendera ndodo kumene.

Koma sikuti anthuwa adabadwa nkhalamba chotere, adali anyamata achichepere; ali ophunzira pa Chaminade zaka zimenezo. Lero si anthu wamba. Ena ndi maloya, madotolo, ansembe, akatswiri a zasayansi ndipo ena ndi aphunzitsi. Ndianthu ofunikira kwambiri mu dziko muno panopa ndipo kupanda ena mwa iwo, dziko lathuli silingayende.

Ambiri, monga wolembayu, adalephera kukhulupirira atalinganiza anthuwa ndi maonekedwe a sukuluyi, poti zipupa zake zimaoneka zosuluka ndi zoderereka.

Ndipo pamene nthawi imakwana 8:50, ambuye Martin Mtumbuka a dayosizi ya Karonga omwe adali mlendo wolemekezeka, adalindiridwa ndianthuwa komanso chinantindi cha anthu chomwe chidali chitasonkhana mu chisangalalo. Chifukwa chawo chosangalalila chidali chimodzi: Chaminade idali itakwanitsa zaka 50.

Ena amene adafika kuchisangalalochi sadaphunzire nawo pasukuluyi. Koma amapita kumatchalichi, kuzipatala komanso kusukulu komwe amatumikiridwa ndi zipatso za sukulu ya Chaminade, yomwe eni ake amayitcha “sukulu ya a namatule”.

Ndipo polankhula pamwambowu pomwe padafika ambuye Joseph Mukasa Zuza a dayosizi ya Mzuzu, mkulu woyang’anira zamaphunziro mu chigawo cha kumpoto, mfumu yayikulu Kyungu ya Ankhonde komanso anthu ambiri a ulemu wawo, a Mtumbuka adapempha anthu onse amene adafika pamalowo kuti alingalire mozama momwe angathandizire kukulitsa Ekileziya Katolika m’dziko muno.

“Tili pa chikondwerero lero chifukwa anthu ena akutali adadzipereka kuti Chaminade [sekondale sukulu] imangidwe. Tizifunse lero zomwe tachitapo potukula mpingo wathu.”
Iwo adayamikira Chaminade ponena kuti yakwanitsa kusula anyamata ambiri aphindu omwe panopa ndi nzika zodalirika komanso zoopa Mulungu. Adayamikiranso a bulaza George Dury a chipanu cha Marianist omwe adali mphunzitsi wamkulu woyamba pa sukulu ya Chaminade komanso a Jobidon ndi a St. Denis omwe adavomereza ndi kuthandizapo kwambiri kuti sekondaleyi imangidwe pansi pa maulamulilo awo ngati oyendetsa dayosizi ya Mzuzu.

A Mtumbuka adapempha mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi a Moses Wanda kuti akhale a chilungamo komanso oteteza zomwe mpingo wa Katolika umafuna kuti zidzisatidwa. Iwo adati masiku ano achinyamata ambiri akuonengeka chifukwa chotengera ufulu wachibadidwe pamgong’o komanso m’dzina la fashoni. Adaopseza kuti sadzalola kuti ophunzira amakhalidwe oyipa azipezeka mu sukulu za mu dayosizi yake.

“A Wanda, mukhale a chilungamo. Ngati kuli mvula nenani kuti ndi nthawi ya mvula, ndipo kukakhala dzuwa nenani kuti kuli dzuwa basi. Musalole wophunzira aliyense kuti atiwonengere mbiri yabwino yasukuluyi.”

“Ngati pali wophunzira amene akuganiza kuti angapose ndi kuvutitsa dayosizi yathu, muchotseni! Koma ziwani kuti aphunzitsinu simungatero ngati muli ndi makhalidwe oyipa. Choncho inunso, ngati aphunzitsi, muyenera kupereka zitsanzo zabwino kwa ophunzira anu.” Adatero a Mtumbuka.

Adapemphanso anthu onse omwe adaphunzira pa Chaminade kuti azithandiza sukuluyi kuti ipitirire kupita patsogolo.

Ndipo mphunzitsi wamkulu pa Chaminade, a Moses Wanda, adati Chaminade idakali imodzi mwa sukulu zopambana kwambiri m’Malawi muno. Malingana ndi a Wanda, ophunzira onse adakhoza mayeso awo a J.C.E chaka chatha ndipo a folomu folo adakhoza ndi 95 peresenti. Iwo adati chaka chatha Chaminade idatumiza ophunzira makumi awiri ku yunivesite ya Malawi komanso asanu ndi m’modzi ku yunivesite ya Mzuzu.

A Wanda adati pakali pano Chaminade yakhazikitsa ndondomeko yija pachingerezi amaitcha Strategic Plan yomwe idziwatsogolera momwe ayendetsere Chaminade kuyambira chaka chino mpaka chaka cha 2022. Panthawiyi, a Wanda adati mwa zina, awonjezera nyumba zina zoti ophunzira azigonamo komanso kuthandiza ophunzira awo kuti azikhala osangalala pasukuluyi.

Mfumu yayikulu Kyungu idayamikiranso Chaminade ponena kuti mu zaka makumi asanu zomwe sukuluyi yakhala pakati pawo yapangitsa kuti anthu a m’boma la Karonga akhale anthu onyadira chifukwa cha zipatso zomwe sukuluyi yatulutsa. Adakumbutsa ophunzira onse kuti dziko la Malawi likufuna anthu ophunzira komanso a makhalidwe abwino.

“Ndikufuna kukupemphani kuti mukhale oziletsa chifukwa kuli matenda oopsa a Edzi. Khalani odekha ndipo musathamangire kukwatira msanga kuti muzavale mikanda yoyera.” Adalangiza motero a Kyungu.

Sekondale ya Chaminade adayimanga ndi mabulaza a chipani cha Marianist m’chaka cha 1962 ndipo anthu odziwika kwambiri m’dziko muno monga Kinnah Phiri yemwe ndi mphunzitsi watimu ya mpira ya dziko lino komanso a Richard Banda omwe ndi mwamuna wake wa pulezidenti wa dziko lino mayi Joyce Banda adaphunzira pasukuluyi.

No comments:

Post a Comment